Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu asanu ndi awiri afa ndi Bomba

$
0
0

Anthu asanu ndi awiri afa mayi wina ataphulitsa mabomba pamalo ena okwelera bus mumzinda wa Damaturu mdziko la Nigeria.

Malipoti a apolisi ati pachiwembucho,anthu makumi atatu 30,avulala.

Padakali pano, palibe gulu lomwe lawulula kuti ndi lomwe latuma mayiyo kuti achite chiwembucho, koma anthu akukayikira zigawenga za Boko Haram zomwe zakhala zikusowetsa mtendere mderalo masiku apitawa, kuti ndi zomwe zatuma mayiyo yemwenso wafera pomwepo.

Mayiyo akuti anafika pamalowo pagalimoto, ndipo analowa mchigulu cha anthu omwe anali pamsika omwe uli pafupi ndi malowo pomwe waphulitsa mabombawo.

Anthu okwiya atentha thupi la mayiyo atafa kale.

Anthu zikwizikwi aphedwa paziwembu zomwe gululo lakhala likuchita mmalo osiyanasiyana mdziko la Nigeria ndinso mmayiko oyandikana nawo,ndipo anthu oposa 3 miliyoni athawa nyumba zawo.

Gululo lidayamba kuchitira anthu ziwembu mchaka cha 2009 pofuna kukakamiza boma kuti livomereze kuti dziko la Nigeria lidziyendetsedwa ndi malamulo achisilamu.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>