Quantcast
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Bungwe la CADECOM Layamikira Boma Pokhazikitsa Ndondomeko Zabwino za Ngozi Zogwa Mwadzidzi

Bungwe lowona zachitukuko mu mpingo wakatolika la Catholic Development Commission CADECOM mdziko muno, layamikira boma kamba kokhazikitsa ndondomeko zomwe zithandize dziko lino kulimbana komanso  kupilira ku ngozi  zogwa mwadzidzidzi.

Mlembi wamkulu m’bungweli a Carsterns Mulume, ndiwo  alankhula izi loweruka pa mwambo okhazikitsa ndondomekoyi mdziko muno omwe unachitikira pasukulu ya Pulayimale ya Chimwala m’boma la Mangochi.

A Mulume ati kwa nthawi yayitali, boma komanso mabungwe akhala akuthandiza anthu mdziko muno pangozi zogwa mwadzidzidzi popanda ndondomeko zothandiza kuti ntchitoyi izigwiridwa bwino, ndipo ati izi zimachititsa kuti magulu onse othandiza azingochita zofuna zawo.

‘Ku boma ku nthambi yoyang’anira za ngozi zogwa mwadzidzidzi koma vuto lomwe lilipo ndi lakuti nthambiyi imapatsidwa ndalama zochepa zomwe zimakhala kovuta kugwiritsa ntchito ngozi zikagwa,’anatero a Mulume.

Iwo apempha boma kuti liyike ndalama zokwanira kuthumba la nthambi yolimbana ndi ngozizi ndi cholinga choti dziko lino lizitha kuthandiza anthu okhudzidwa mwachangu komanso kuti papezeke njira zopewera mavuto odza chifukwa cha ngozizi.

Iwo ati, ‘ndondomekoyi ithandiza kamba koti magulu osiyanasiyana azikhala pamodzi ndi kukonza dongosolo loyenera kutsata ngozi zadzidzidzi zikagwa.’

Nthambiyi imagwira ntchito ndi ofesi ya Pulezidenti.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>