Mtsogoleri wampingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco,wayamikira akhristu a mpingowu mdziko la Japan chifukwa cholimba pa chikhulupiliro chawo,ngakhale akhala akukumana ndi mavuto osiyanasiyana kuphatikizapo achilengedwe.
Papa Francisco,amalankhula izi lachisanu pa mkumano omwe anali nawo ndi maepiskopi a mdziko la Japan-lo omwe ali paulendo okacheza kulikulu la mpingowu omwe maepiskopi mumpingowu padziko lonse amakhala nawo pakatha zaka zisanu.
Iye wawuza ma episkopiwo, kuti kulimba mtima pachikhulupiliro komwe akhristu a mdzikolo akhala akuwonetsa,ndi phunziro lalikulu kwa akhristu onse mumpingowu kuti asamafowoke pa chikhulupiliro chawo.
Mtsogoleri wampingo wakatolikayu anatchulapo ngozi ya tsunami, nkhondo yomwe idawononga dzikolo zaka makumi asanu ndi awiri zapitazo komanso kupezeka kwawo pakati pa anthu osakhulupilira Mulungu, kuti ndi zina mwa zovuta zomwe iwo akhala akupilira.
Iye wayamikiranso maepiskopiwo chifukwa cha ntchito yayikulu yomwe akhala akugwira potukula maphunziro, umoyo komanso za chifundo kwa anthu osowa ndi zina zambiri.