Pulezidenti wa dziko la Tanzania a Jakaya Kikwete walamula apolisi m’dzikolo kuti afufuze mwansanga za kuphedwa kwa wamsembe wina wa Mpingo wa Katolika m’dzikolo.
Pulezidenti Kikwete walamula izi pambuyo pa imfa ya wamsembe wina Bambo Evaristus Mushi yemwe adaphedwa pamalo ena pa chilumba cha Zanzibar.
Mkulu wa apolisi m’dzikolo a Saidi Mwema wadzudzula anthu omwe anakonza chiwembucho ndipo wati akukhulupirira kuti anthuwo achita izi mwina kamba ka zifukwa za kusiyana kwa zipembedzo kapena zifukwa za ndale.
Bishop Augastine Shao waderalo wati atsogoleri ambiri a mipingo kuderalo ali ndi mantha aakulu kamba ka zomwe zachitikazo.
Malinga ndi Bishop Shao, anthu omwe achita chiwembucho akhala akutumiza mauthenga apa lamnya kwa akuluakulu a Mpingo wa Katolika kuderalo kuwaopseza kuti apitiriza kukonza ziwembu za mtunduwu.
Kuphedwa kwa Bambo Mushi a zaka 56, kwadza pambuyo pa kuwomberedwa kwa wamsembe wina yemwe adawomberedwa patsiku la Khirisimisi ndipo padakali pano adakali m'chipatala.
Anthu enanso akuti adawotcha ma tchalitchi asanu pa chilumbacho
chaka chatha.
“