Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Pulezident Jonathan Asayinira Mgwirizano ndi a Buhari

$
0
0

Pulezidenti Goodluck Jonathan ndi yemwe anali  mkulu wa asilikali a gulu la nkhondo a dziko la Nigeria a Muhammadu Buhari asayinirana mgwirizano wakuti sipadzakhala ziwawa pambuyo pa zotsatira za chisankho zomwe zikuyembekezeka kuchitika mdzikolo Loweruka sabata ino.

 

Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, atsogoleriwa alonjeza kuti adzavomereza zotsatira za chisankhocho ndipo apempha otsatira awo kuti adzapewe ziwawa pambuyo pa zotsatirazo.

 

Izi zachitika kamba koti anthu 800 anaphedwa pambuyo pa zotsatira za chisankho cha mchaka cha 2011 chomwe chinachitika mdzikolo.

 

Atsogoleri onse amene akupikisana nawo pa chisankhochi lachinayi atsiriza misonkhano yawo yokopa anthu kuti adzawavotere.

 

Pa chisankhochi atsogoleri khumi ndi anayi 14 ndi amene akonzeka kupikisana nawo pa udindo wa Pulezidenti.

 

 

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>