Mtsogoleri wampingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco, wavomereza mayina a maepiskopi a mmayiko makumi anayi omwe mabungwe a maepisikopi mmayikowa asankha kuti akawayimilire pa msonkhano wachiwiri wa maepiskopi okambirana nkhani zokhudza banja.
Papa Francisco wavomereza nthumwizi kumsonkhanowu, pambuyo povomereza zina zochokera mmayiko makumi atatu mmwezi wa January.
Msonkhanowu, ukuyembekezeka kudzachitikira kulikululo m’mwezi October chaka chino.
Zina mwa nthumwi zomwe zikuyembekezeka kudzakhala nawo pa msonkhanowo zomwe Papa Francisco wazivomereza posachedwapa ndi Cardinal Reinhard Marx, Cardinal Jorge Urosa Savino wa mdziko la Caracas komanso Arkbishopu Philip Tartaglia waku Glasgow ku England.