Mtsogoleri wampingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco, wapepesa mabanja omwe ataya abale awo pangozi ya ndege yomwe yachitika lachiwiri mdziko la France.
Ndegeyo yomwe ndi ya mdziko la Germany, idanyamuka 9 koloko mmawa pabwalo la Barcelona mdziko la Spain, paulendo wopita ku France.
Pakadali pano chomwe chachititsa ngoziyo sichikudziwika, ndipo ntchito yofufuza ikupitilira.
Atsogoleri a mmayiko a France, Germany komanso Spain, akuyembekezeka kufika pamalo pomwe ndegeyo yagwera.