Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Nyumba Zofalitsa ndi Kutsindikiza Nkhani Zili ndi Udindo Wofalitsa Nkhani za Matenda

$
0
0

Unduna wa zaumoyo wati nyumba zofalitsa komanso kutsindikiza nkhani zili ndi udindo waukulu wofalitsa nkhani zokhudza matenda osiyanasiyana m’dziko muno.

Nduna mu undunawu Wolemekezeka Dr Jean Kalirani anena izi Lachinayi mu mzinda wa Lilongwe pa msonkhano wa akuluakulu anyumba zofalitsa ndi kusindikiza nkhani komanso mabungwe omwe ndiwokhudzidwa ndinkhani zaumoyo.

Dr Kalirani ati mkumanowu upindula kwambiri kamba koti ulumbikitsa ubale pakati pawo zomwe zithandize kutumikira bwino mtundu wa  a Malawi.

‘Nkumanowu ndi wofunika kwambiri kamba koti nyumbazi zimagwira ntchito yodziwitsa anthu zochitika za mdziko,’anatero a Kalirani.

Iwo ati undunawu umakhala ndi mauthenga osiyanasiyana okhudza za umoyo oti anthu adziwe, choncho ndi udindo wa nyumbazi  kufalitsa mauthengawo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>