Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Bungwe la Cadecom Layamikira Bungwe la YCW

$
0
0

Bungwe lowona za chitukuko mu mpingo wa Katolika la Cadecom, layamikira achinyamata a mgulu la YCW mu Parish ya Kaggwa Woyera ku Archdayosizi  ya Lilongwe popereka katundu wosiyanasiyana ku bungweli woti athandizire anthu omwe akhudziwa ndi ngozi ya kusefukira kwa madzi m’dziko muno.

A Carstens Mulume ndiwo alankhula izi Lachinayi ku likulu la mpingowu ku Lilongwe polandira katundu wosiyanasiya yemwe achinyamatawa apereka.

Iwo ati bungwe lawo lomwe likugwira ntchito yogawa zinthu zosiyanasiyana kwa anthu omwe akhuzidwa ndi madzi osefukira, liwonesetsa kuti thandizoli lafikiradi anthu oyenerera.

Pamenepa a Mulume apempha achinyamata ena mdziko muno kuti atengerepo chitsanzo pa zomwe achinyamatawa achita.

Mmodzi mwa mamembala a gululi a Collins Mkwende ati anawona kuti ndi kofunika kuti achitepo kanthu  pa vuto lomwe anthu mdziko muno anakumana nalo.

‘Titakhala pansi tinagwirizana kuti titengepo gawo posonkherana kuti tipeze katundu yemwe tapezayu,’ anatero a Mkwende.

Bungweli linapeza katunduyu ndi thandizo lochokera ku Parishi yawo ya Kaggwa Woyera ndipo lalimbikitsa achinyamata kuti akhale ndi mtima wogawana ndi anzawo akachepekedwa.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko