Unduna wa zaumoyo walangiza anthu mdziko muno kuti apewe mchitidwe omvera zinthu zomwe zikupereka phokoso lopitilira muyeso pofuna kupewa matenda a khutu.
Nduna ya za umoyo Dr. Jean Kalirani ndi yomwe yapereka langizoli Lachisanu pa chipatala cha Queen Elizabeth Central mu mzinda wa Blantyre pamwambo wokumbukira kufunika kwa makutu.
Dr Kalirani ati anthu ambiri amakonda kutsekula zoyimba mopitilira muyeso, kumvera nyimbo pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono zomvera paulendo ndi zina zambiri zomwe zikukolezera matenda a khutu.
‘Mavuto ena a kusamva amabwera chifukwa chokonda kumvera zinthu zokwezedwa kwambiri zomwe nthawi zina zimadzetsa mavuto a makutu,’anatero a Kalirani.
Iwo alimbikitsa anthu kuti akaona kuti mkhutu mwawo muli vuto asamazengereze koma azithamangira ku chipatala.
Pothilirapo ndemanga dotolo wowona za matenda a khutu pa chipatalacho Dr Wakisa Mulwafu, wati mdziko muno muli anthu pafupifupi 650 sauzande omwe amavutika ndi nthendayi zomwe zikutanthauza kuti vutoli ndi lalikulu kwambiri.
Padakali pano boma linakhazikitsa chipatala chapadera ku chipatala chachikuluchi ndi cholinga choti anthu amene amavutika ndi nthendayi azithandizika.