Bungwe la atolankhani lolimbana ndi matenda a Edzi la Journalist Against Aids, lati matendawa m’dziko muno angachepe ngati a mipingo atadzipereka pofalitsa kuopsa kwa matendawa akakhala m’makachisi awo.
Mkulu wa bungweli a Christopher Bauti, ndi yemwe wanena izi Lachisanu mu mzinda wa Lilongwe, pa mkumano watsiku limodzi wa bungweli ndi akuluakulu a mipingo yosiyanasiyana.
A Bauti ati amipingo angatengepo mbali yayikulu pa ntchito yofalitsa uthenga wokhudza kuwopsa kwa matendawa kudzera mu magulu osiyanasiyana omwe akhristu amakumana.
‘Tinaona kuti mbali imodzi yofalitsira ma uthenga a matendawa ndi kudzera mwa akuluakulu a mipingo kamba koti munthu aliyense amakhala ndi nthawi yopita kukapembedza,’ anatero a Bauti.
Iwo ati ndi wokondwa kuti mmipingomo muli magulu osiyanasiyana zomwe zithandize mu kafalitsidwe ka ma uthengawa.
Bungweli lakhala likugwira ntchitoyi ndi mabungwe, akuluakulu a ndale ngakhalenso boma la dziko lino pofuna kuwonetsetsa kuti chiwerengero cha matendawa chikuchepa.