Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Chipatala cha Bwaila Fistula Care Centre Achiyamikira Pokwaniritsa Zina mwa Zolinga Zake

$
0
0

Chipatala chomwe chimathandiza amayi omwe anapezeka ndi vuto la Fistula cha Bwaila Fistula Care Centre mu mzinda wa Lilongwe, achiyamikira kamba kokwaniritsa zina mwa zolinga zake polimbana ndi vutoli.

Mmodzi mwa amayi omwe adali ndi vutoli ndipo anachira mayi Sophie Yusufu  a m`mudzi mwa Mkanda m’boma la Mchinji ndi yemwe wayamikira ntchito za chipatalachi lachisanu pambuyo pa maphunziro a tsiku limodzi owaphunzitsa m’mene angafalitsire uthenga wokhudza matenda a Fistula.

Iwo ati akhala akukumana ndi mavuto aakulu asadachire ku matendawa kuphatikizapo  kusalidwa ndi anthu.

Mayi Yusuf anati, ‘Ineyo nthendayi inandivuta kwambiri ndipo banja langa mpaka linatha komanso anzanga anasiya kucheza nane.’ 

Pamenepa mayi Yusuf alimbikitsa amayi kuti asamadzibise akaona zizindikiro za matendawa koma azithamangira ku chipatalachi kamba koti matendawa ndi ochizika.

Polankhulapo mkulu wa chipatalacho a Magret Moyo ati matendawa amabwera kamba ka vuto la uchembere.

‘Pamene mzimayi wapita ku chipatala mochedwa amatha kuvulala kamba koti mwana yemwe amakhala kuti wanyamula amawononga ziwalo zina zomwe zimabweretsa vuto la matendawa,’anatero Mayi Moyo.

Iwo ati odwala pafupifupi 250 amene akhala akubwera pa chipatalachi akhala akuthandizidwa ku matendawa.

Ku maphunzirowa kunabwera amayi omwe anachira ku matendawa ndi cholinga choti akabwerera akapereke uthenga kwa anzawo.

 

 

 

 

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>