Mtsogoleri wa mpingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco wati akhristu angathe kupewa mayesero a dziko lapansi potsatira makhalidwe omwe Yesu Khristu mwini adawonetsa.
Papa Francisco wanena izi Lamulungu pa nsembe ya Misa ya kanjedza yomwe anatsogolera pa bwalo la St.Peters Square ku likulu la mpingowu ku Vatican.
Mmawu ake mtsogoleri wampingo wakatolikayu wati padziko lapansi, pali miyoyo iwiri yomwe ndi kukonda Mulungu ndi mtima onse komanso kukonda zapansi pano monga chuma ndi zina zomwe Yesu Khristu mwini adazipewa pamene satana amkamuyika mmayesero.
Iye wati akhristu, angathenso kugonjetsa mayesero omwe amakumana nawo pokhala ndi mtima wokonda Mulungu, wodzichepetsa komanso wofuna kutumikira ena nthawi zonse monga Yesu Khristu adawonetsa munthawi yonse yautumiki wake.