Akhristu awalangiza kuti akhale olimba pa chikhulupiliro pofuna kuti azitha kugonjetsa adani achikhulupiriro chawo.
Mmodzi mwa ansembe otumikira ku Seminary ya Nankhunda mu dayosizi ya Zomba ya mpingo wa Katolika bambo Patrick Kamba ndi omwe apereka langizoli Loweruka pambuyo pa m’bindikiro wa tsiku limodzi wa anthu otumikira ku studio ya Zomba ya Radio Maria mu dayosiziyo.
Mmawu awo, bambo kamba ati moyo wa munthu umakhala ndi adani asanu amene amalanda ufulu wake, ndipo ati ena mwa iwo, amakhala iye mwini pamene nthawi zina pamapezeka kuti wadzitemberera komanso kuganiza zambiri zongofuna kudzisangalatsa.
Pamenepa iwo ati kutsatira Mulungu ndi chikhulupiriro chonse ndi njira yokhayo yogonjetsera adaniwa.