Ophunzira mmodzi wafa ndipo ena oposa zana limodzi, avulala pa sukulu ina ya ukachenjede mu mzinda wa Nairobi m’dziko la Kenya, transifoma ya magetsi itaphulika pafupi ndi sukuluyo.
Ophunzirayo wafa pachipwilikiti chomwe chinabuka, pomwe anthu amalimbirana kutuluka mzipinda zawo pa sukuluyo poganiza kuti pasukuluyo, pafika achiwembu.
Anthu m’dzikolo akukhala mwa mantha, potsatira imfa ya anthu 148 omwe anaphedwa pa chiwembu chimene gulu la zigawenga za Al-Shabaab za m’dziko la Somalia, zinachira pa sukulu ina ya ukachenjede mdzikomo.
Pakadali pano dziko la Kenya lalamula kuti mzika za dziko la Somalia zomwe zikukhala pamalo ena osungira anthu othawa kwawo mdzikolo zibwelere mdziko lawo.
Pa malopo pali anthu oposa 500 sauzande a m’dziko la Somalia, omwe ena mwa iwo akhalapo kwa zaka zoposa makumi awiri.
Anthu omenyelera ufulu wa anthu mdziko la Kenya adzudzula dzikolo kaamba ka ganizo lofuna kusamutsa anthuwo.