Lipoti latsopano lomwe likulu la mpingo wakatolika latulutsa, lasonyeza kuti chiwerengero cha akhristu a mpingowu chakwera kwambiri mu zaka zisanu ndi zitatu zapitazi.
Lipotilo lati kuyambira mchaka cha 2005 kufika chaka cha 2013, anthu 12 mwa anthu 100 aliwonse, amalowa mpingo wakatolika, zomwe zachititsa kuti chiwerengero cha akhristu mumpingowu pakadali pano chipose 1biliyoni 254 miliyoni.
Chiwerengerochi ati chakwera kwambiri maka mmayiko amu Africa, m’mene tsopano muli akatolika 206 miliyoni.
Lipotili likusonyezanso kuti chiwerengero cha a sisiteri ndi a semino pa dziko lonse chikutsika kwambiri.
Posachedwapa, Episkopi wa dayosizi ya Karonga Ambuye Martin Mtumbuka,omwenso ndi mkulu oyang’anira za maphunziro kubungwe la maepiskopi mdziko muno, anadandaula chifukwa cha kuchuluka kwa achinyamata omwe akumachotsedwa msukulu zosulira ansembe mdziko muno, ophunzira awiri akusukulu yosulura ansembe ya Kachebere m’boma la Mchinji atachotsedwa pa sukuluyo.