Anthu pafupifupi zikwi zisanu,mdziko la South Africa lachinayi anachita ziwonetsero zokwiya ndi ziwembu zomwe mzika zina za dzikolo zakhala zikuchitira anthu a mmayiko ena omwe akukhala mdzikolo.
Anthuwa anachita ziwonetserozo mtsogoleri wa dzikolo Jacob Zuma, atawuza aphungu akunyumba ya malamulo kuti ziwembu zomwe anthu ena akhala akuchitira alendo mdzikolo, ndi zosavomerezeka.
Pakadali pano anthu asanu, ndi omwe atsimikizika kuti afa pa ziwembu zomwe zakhala zikuchitika mdzikolo, ndipo boma la dziko lino latumiza bus zisanu ndi imodzi zoti zikasamutse mzika za dziko lino zomwe zili mdzikolo, maka zomwe zili ndi chidwi chofuna kubwelera kuno kwawo.
Anthu ambiri omwe akusowa ntchito mdzikolo, amadzudzula anthu a mmaiko ena kuti ndi omwe akugwira ntchito zomwe eni dzikolo akuyenera kumagwira.
Pakadali pano anthu 24 mwa anthu 100 aliwonse mdzikolo akusowa ntchito.