Mwana wina wa chipembedzo cha chikhristu mdziko la Pakistan waphedwa potenthedwa ndi moto wa mafuta a Petulo atapezeka akuwuza anthu kuti iye ndi mkhristu.
Malipoti ati mwanayu Noman Masih, anali wa zaka khumi ndi zitatu zakubadwa ndipo wakhala akunena izi mosabisa zomwenso anthu ena amakwiya nazo.
Anthu awiri omwe sakudziwika,ndi omwe apha mwanayo.
Padakalipano, mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wa akhristu m’dzikomo Mervyn Thomas, wati bungweli ndi lokhudzidwa kwambiri ndi imfa ya mwanayo.
Iye wapempha boma la dzikolo kuti lithandize kupereka chitetezo chokwanira kwa akhristu amene akuzunzidwa munjira zosiyanasiyana ndi anthu odana ndi chipembedzochi.
Dziko la Pakistan ndi lili ndi chiwerengero chachikulu cha anthu otsatira chipembedzo cha chisilamu.