Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Bungwe la ECM lakonza Mgonero Pofuna Kupeza Ndalama Zoyendetsera Kachebere Major Seminary.

$
0
0

Bungwe la ma episkopi mdziko muno la Episcopal Conference of Malawi ECM, kupyolera mu komiti yake yofufuza chuma choyendetsera sukulu yosulira ansembe ya Kachebere, lakonza mgonero pofuna kupeza ndalama zoyendetsera chikondwelero cha zaka 75 cha sukuluyi.

Mwambowu udzachitika lachisanu pa 24 April ku Bingu International Conference Centre (BICC) mumzinda wa Lilongwe, pomwe bandi ya Kalimba ikuyembekezeka kudzaimba.

Wapampando wasukulu zosulira ansembe kubungweli mdziko muno Ambuye Martin Mtumbuka,omwenso ndi wachiwiri kwa wapampando wa bungwe la ECM, adatsekulira chikondwero choti sukuluyi yatha  zaka 75 ikugwira ntchito zake pa 10 January chaka chino, ndipo mwambo waukulu okondwelera sukuluyi uchitika mmwezi wa October chaka chino.

Kachebere Major Seminary inatsekulidwa mchaka cha 1939 ndipo tsopano yakwanitsa zaka 75 ikugwira ntchito yosula ansembe komanso atsogoleri osiyanasiyana.

Kale sukuluyi inkapereka maphunziro ake kwa achinyamata ochokera mmaiko a Zambia ndi Malawi ndipo pano ophunzira a mdziko muno okha ndi amene amalandira maphunziro a utumikiwu kuchokera mmadayosizi onse asanu ndi atatu a mpingowu.

Mmawu awo,Ambuye Mtumbuka apempha akhristu ndi anthu onse akufuna kwabwino kuti athandize pamwambowu poyang’anira ntchito yaikulu yomwe sukuluyi imagwira pokonzekeretsa anthu unsembe.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>