Boma la dziko la Burundi lati silibwenzera anthu omwe akukhudzidwa mugulu lomwe lakhazikitsidwa lofuna kuchotsa pampando Pulezidenti Pierre Nkuruzinza kuti asayimenso pa chisankho chomwe chikuyembekezeka kuchitika mdzikolo.
Malinga ndi uthenga omwe bomali latulutsa malamulo agwira ntchito kuti chilungamo chidziwike.
Malipoti a wailesi ya BBC ati ziwonetsero zikupitilira ku likulu la dzikoli ku Bujumbura pomwe ofesi ya nthumwi ya European Union EU anaponyako zipolopolo.
Mabungwe a EU komanso African Union AU alamula kuti chisankhocho chomwe chikuyembekezeka kuchitika pa mwezi wa mawa pa 26 chisachitike koma Pulezidenti Nkuruzinza wakanitsitsa, iye wati chisankho chikhalepo.
Padakali pano anthu oposa 1 hundred and 5 sauzande athawa mdzikolo kupita ku mayiko oyandikana nawo kamba ka zomwe zikuchitika mdzikolo.