Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Bomba Lapha Anthu Asanu Ndi Awiri Mdziko La Nigeria.

$
0
0

Anthu asanu ndi awiri afa pa msika wina mdziko la Nigeria ndi bomba lomwe linaphulitsidwa pa msikawo.

Malinga ndi malipoti a BBC aka ndi kachiwiri sabata ino izi kuchitika ku mpoto kwa dzikoli pomwenso anthu ena asanu ndi anayi anaphedwa pa tawuni ina ya Yobe pomwe mzimayi wina yemwe anavala bomba anaphulitsa pa malo ena okwelera bus.

Padakali pano amene achita izi sadadziwike koma zigawenga za gulu la chisilamu za Boko Haram ndi zomwe akuziganizira kuti zikukhudzidwa ndi ziwembuzi.

M’mwezi wa January chaka chino anthu 19 anafa ndipo ena ambiri anavulala ndi bomba lomwe anaveka msungwana wina wa zaka khumi lomwe linaphulitsidwa mbali yomweyi ya dzikolo.

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>