Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Ark Episkopi Gabriel Anokye Wasankhidwa Kukhala Mkulu Wa Caritas International mu Africa.

$
0
0

Ark Episkopi wa mdziko la Ghana Gabriel Justice Yaw Anokye wasankhidwa kuti akhale mtsogoleri watsopano wa bungwe la Caritas International wa mmayiko a kuno Africa.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican Ambuye Anokye awasankha ku  msonkhano wa pachaka wa bungweli omwe unachitikira mu mzinda wa Rome mdziko la Italy.

Ku msonkhanowu Kadinala Luis Tagle wa mdziko la Phillipines anasankhidwanso kukhala mtsogoleri watsopano wa bungweli pa dziko lonse yemwe anatenga udindo wa Kadinala Oscar Rodriguez Maradiaga omwe akakhala pa udindowu kwa zaka ziwiri.

Polankhulapo mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha atsogoleri atsopanowa kuti alimbike pa ntchito yawo pofuna kuti zipatso za bungweli zifalikire mmadera onse a pa dziko lapansi.

Ku msonkhanowu kunafika nthumwi pafupifupi 400 zochokera mmayiko onse omwe ali mu bungweli.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>