Dziko la Nigeria likusunga amayi ndi ana omwe apulumutsidwa mmanja mwa zigawenga za Boko Haram ku malo ena a asilikali pofuna kuti liziwasamalira mwanjira zosiyanasiyana.
Kumalo a asilikaliwo,amayiwo azilandira uphungu pankhani zosiyanasiyana ndi cholinga choti ayiwale nkhanza zomwe akhala akukumana nazo.
Dzikolo latinso lili ndi nkhawa pomwe likukayikira kuti ena mwa amayiwo atha kukhala ataphunzira moyo wankhanza kwa zigawengazo.
Malipoti ati panthawi yomwe amayiwo amasungidwa mmisasa ya boma amai ena amawonetsa zizindikiro zoti akumalumikizana ndi mamembala a mgulu la zigawengalo