Pulezidenti wadziko lino Proffesor Arthur Peter Mutharika wapempha a Malawi onse kuti agwirane manja pofuna kupititsa patsogolo chitukuko cha dziko lino.
Proffesor Mutharika wanena izi lachisanu pa mwambo otsekulira chiwonetsero cha za malonda cha nambala 27 ku Chichiri Tradefare grounds mu mzinda wa Blantyre.
Iye wapempha onse ochita malonda kuti agwirane manja ndi boma m'malo molozana chala pa zomwe sizikuyenda bwino.
“Nthawi yolozana zala pa momwe zinthu zikuyendera m'dziko muno inatha, anthu akuyenera kudzipereka pa chitukuko cha dziko lino,” anatero a Mutharika.
Malinga ndi Proffessor Mutharika chitukuko cha dziko lililonse chimadalira kudzipereka kwa m'zika za dzikolo pa ntchito monga zamalonda.
A Mutharika ati, “amalawi akuyenera kukhala oyamba kugula katundu wawo zomwenso zingathandize kutukula chuma cha dziko lino.”
Polankhula pa mwambowo nduna ya zamalonda a Joseph Mwanamvekha ati unduna wawo uwonetsetsa kuti magawo onse ochita malonda akugwirira ntchito limodzi kuti chitukuko cha dziko lino chipitilire kukwera.
Pa mfundoyi, iwo apempha ochita ma bizinezi akuluakulu kuti agwirane manja ndi a mabizinezi ang'onoang'ono kuti athe kutukulana iwo eni pawokha.
Ma kampani asanu omwe ndi a Admarc, Mosanto Malawi, Pharmanova, Sky Furniture komanso nthambi yowona mpikisano pamalonda Competition and Fair Trading Commission alandira mphotho kamba kochita bwino mu magawo osiyanasiyana a zamalonda.
Ma kampani oposa mazana awiri (200) a kuno ku Malawi kudzanso anayi ochokera mmayiko a India, Tanzania, Zimbabwe ndi Kenya ndi omwe awonetsa chidwi chochita nawo chiwonetserochi chaka chino.
Chiwonetsero cha malondachi chomwe chayamba pa 22 May 2015chidzatha pa 30 May chaka chino.
Panthawiyi anthu ndi mabungwe ochita malonda akhala akuwonetsa zomwe amachita komanso kuthandizana za momwe angapititsire patsogolo ntchito za malonda.