Mwambo okhazikitsa malemu Sister Ireen Stefani kukhala odala wachitika loweruka lapitali mu ark dayosizi ya Nairobi mdziko la Kenya.
Kadinala Polycarp Pengo yemwenso ndi arkepiskopi wa dayosizi ya Dar es Salaam mdziko la Tanzania ndi yemwe anayimilira mtsogoleri wa mpingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco pa mwambo wa nsembe ya ukaristia yomwe anatsogolera ndi Kadinala John Njue wa arkidayosizi ya Nairobi.
Miyambo yokhazikitsa atumiki a Mulungu omwe adadzipereka kwathunthu pa moyo wawo potumikira Mulungu komanso anthu kukhala odala, yakhala ikuchitikira ku likulu la mpingowu ku Vatican, koma mpingo unaganiza zopereka mphamvu kudayosizi komwe munthuyo adatumikira komanso kumwalilira kuti izipereka mdalitsowu.
Thupi la malemu Sister Ireen Stefani lachotsedwa lamulungu mmanda akale, ndipo layikidwa mmanda atsopano omwe akhazikitsidwa kukhala opatulika.
Akhristu tsopano adzigwiritsa ntchito malo a pamandawo popempha chifundo cha Mulungu pankhani zosiyanasiyana.
Pamwambo okhazikitsa malemuwo kukhala odala, Kadinala Pengo anawerenga kalata yomwe likulu la mpingowu latumiza kudayosizi ya Nairobi, yofotokeza za moyo wa Sister Stefani omwe adafika mdzikolo mchaka cha 1915 ndipo adamwalira mchaka cha 1930 ali ndi zaka 39 zakubadwa.