Sister Ellen Chikwawa a chipani asisteri cha Sisters of the Blessed Virgin Mary SBVM, amwalira.
Sister Chikwawa,omwe amwalira la Mulungu madzulo, anabadwa mchaka cha 1940 mmudzi mwa Chimatila mdera la mfumu yaikulu Mulumbe ku Namitembo parishi mu dayosizi ya Zomba.
Iwo adayamba moyo wachipani mchaka chaka 1964 ndipo adachita malumbiro awo oyamba pa 8 December mchaka cha 1967,ndipo malumbiro a mpaka kufa adachita pa 8 September mchaka cha 1974.
Malemu Sister Ellen Chikwawa,akhala akutumikira mmalo osiyanasiyana mumpingowu kwa zaka 47 ndipo amwalira ali ndi zaka 74 zakubadwa.
Misa yaulemu yotsazikana nawo, ichitika lachiwiri pa 26 May 2015 ku Mary View m’boma la Chiradzulu.