Mtsogoleri wa dziko la Nigeria GoodLuck Jonathan,akuyembekezeka kupereka udindowu kwa mtsogoleri watsopano Muhamad Buhari lachisanu likudzali atalephera pachisankho cha pulezidenti chomwe chidachitika mdzikolo pa 28 March chaka chino.
Malipoti akusonyeza kuti pulezidenti Jonathan akhala akupereka udindowu kwa a Buhari dzikolo lili mmavuto aakulu azachuma.
Padakali pano ntchito za mtengatenga ndi malonda mdzikolo akuti zaima chifukwa chakusowa kwa mafuta a galimoto komanso ndege.