Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Nthambi ya CCJP ku Vatican Yati Chaka cha 2015 ndi Chofunika

$
0
0

Nthambi yowona za chilungamo ndi mtendere kulikulu la mpingo wakatolika ku Vatican lati chaka cha 2015 ndi chofunikira kwambiri pachitukuko cha mayiko.

Mtsogoleri wa nthambiyi kulikululo Kadinala Peter Turkson ndi yemwe wanena izi mumzinda wa Rome mdziko la Italy pa msonkhano wa masiku atatu wa nthumwi za mmayiko osiyanasiyana zomwe zakhala zikuwunika zitukuko zoyenera kuchitika mzaka khumi ndi zisanu zikubwerazi.

Kadinala Turkson wati pamene chaka chino chili chomaliza kukwaniritsira mfundo za bungwe la United Nations zokhudza chitukuko za Millenium Development Goals, mayiko akuyenera kuwonetsetsa kuti mfundo zina zomwe zingaperekedwe kuti zikwaniritsidwe mzaka zina khumi ndi zisanu zikubwerazi zikwaniritsidwe maka polimbikitsa amayi kutenga nawo mbali.

Padakali pano mfundo 17 za chitukuko ndi zomwe zaperekedwa kuti mayiko akwaniritse pomafika mchaka cha 2025, ndipo pali chiyembekezo choti mfundozi zidzaunikidwa komanso kuvomerezedwa mmwezi wa September chaka chino.

Litawunikira bwino mfundo zatsopano za chitukuko zomwe nthumwi kumsonkhanowo zakonza kuti zivomerezedwe, nthambi ya chilungamo ndi mtendere kulikulu la mpingo wakatolika lapeza kuti mfundo zambiri pa mndandanda wa mfundo 17 zomwe zayikidwa zidzasowa kuyika amayi patsogolo kuti zidzakwaniritsidwe mmayiko.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>