Akhristu awapempha kuti akhale olimba pa chikhulupiliro chawo posiya makhalidwe omwe ndi osiyana ndi mphatso zomwe Mzimu Woyera umapereka .
Nduna ya episkopi wa Arkidayosizi ya Blantyre Monsinyo Bonface Tamani ndi yomwe yapereka pempholi lamulungu ku Parishi ya Mthawira pa nsembe ya misa ya Ulimbitso pomwenso mpingo wa Katolika, umakumbukira Kutsika kwa Mzimu woyera kwa atumiki oyambilira.
Monsinyo Tamani wati ndi zomvetsa chisoni kuti ngakhale Mulungu anatumiza Mzimu woyera, akhristu ambiri akupitiriza kutenga mbali pa zikhalidwe zosiyanasiyana zoipa kuphatikizapo mchitidwe wachinyengo womwe umadzetsa mavuto osiyanasiyana.
Mu uthenga wake Monsinyo Bonface Tamani wati akhristu akuyenera kukhala a Chikondi, Chimwemwe, Mtendere, Ofatsa, Okoma mtima, Okhulupilika ndinso Odziletsa zomwe ndi Mphatso zisanu ndi ziwiri za Mzimu Woyera.
Monsinyo Tamani wapemphanso akhristu omwe alandira sacrament la Ulimbitso kuti adzipereke potenga mbali mu magulu amumpingo kuti mphatso za mzimu woyera zomwe alandira zipindulire anthu ambiri.
Polankhulapo Bambo Lawrence Simbota omwe ndi Bambo mfumu a Parishi ya Mthawira ati ndi okhutira ndi momwe chikhristu chikuyendera ku Parishiyo chifukwa akhristu akudzipereka pothandiza anzawo kudziwa za mpingo wa katolika pomwe zathandiza kuti anthu ochuluka alowe mumpingowu ndi kulandira sakrament la Ulimbitso.