Mwambo oyika m'manda thupi la malemu Sister Ellen Chikwawa wachitika lachiwiri ku likulu la chipani cha Atumiki a Maria Virgo ku Mary View ku Nguludi m'boma la Chiradzulu.
Episkopi wa Dayosizi ya Chikwawa Ambuye Peter Musikuwa ndi omwe anatsogolera mwambo wa nsembe ya misa ya malirowo.
Polankhula ku namtindi wa anthu omwe anabwera kudzapereka ulemu wawo otsiriza kwa malemu Sister Ellen Chikwawa, Ambuye Musikuwa ati imfa ya atumiki a Mulungu imakhala yowawa nthawi zonse poganizira kuti atukimiwa ndi ochepa kuyambira kale.
Iwo apempha ma Sisteri onse kuti apitilire kukhala ogwirizana kuti utumiki wawo ukhale opambana.
Ambuyewa anayamikira ansembe,asisteri komanso akhristu onse kamba kotenga mbali pa mwambo wa maliro a malemu Sr Chikwawa.
Poyankhula kuimilira Chipani cha atumiki a Maria Virgo, Sr Magret Zionga ati malemu Sr Chikwawa anali mtumiki wabwino pakati pawo poti anali mlangizi kwa onse komanso olimbikira ndi odzipereka pogwira ntchito za chipani.
Polankhulapo mmalo mwa aku banja Bambo Lucius Chikwawa omwe ndi mlongo wawo wa malemuwa ati ndi othokoza Mulungu kamba ka mphatso ya moyo wa Sr Chikwawa omwe kwa iwo kupatula kukhala m'bale wawo, anali mtumiki nzawo komanso munthu yemwe amatha kugawana naye zokoma ndi zowawa za mu utumiki wawo ndinso kuti anali mulangizi ndi chitsanzo chabwino ku banja lawo lonse poti iwo anali oyamba kubadwa m'banjali.
Malinga ndi bambo Chikwawa Malemuwa amwalira ndi nthenda yakufa kwa ziwalo komanso Cancer.
Ena mwa omwe anali nawo pa mwambowo ndi nduna ya Arkiepiskopi wa Arkidayosizi ya Blantyre Monsignor Boniface Tamani, Vicar General watsopano wa Dayosizi ya Zomba Bambo Vincent Chilolo, ansembe, asisteri, abulazala ndi akhristu eni ake kuchokera kumadera osiyanasiyana.
Malemu Sr ellen chikwawa anabadwa m`chaka cha 1940 m`mudzi mwa Chimatira kwa mfumu yaikulu mulumbe ku Namitembo parishi mu Dayosizi ya Zomba.