Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mpingo wa Katolika Mdziko la Burundi ndi Wokhudzidwa

$
0
0

Mpingo wakatolika m’dziko la Burundi wati ndi wokhudzidwa ndi momwe zinthu zilili pa ntchito yokonzekera chisankho cha Pulezidenti chomwe dzikolo likuyembekezeka kukhala nacho mwezi wa mawa.

Mpingowu wanena izi kudzera mchikalata chomwe watulutsa pokambapo za momwe zinthu zilili pa ndale mdzikolo.

Mwa zina chikalatacho chatsindika kuti ngati zinthu sizisintha pa ziwonetsero zomwe anthu akupitiliza kuchita posagwirizana ndi ganizo loti m’tsogoleri wa dzikolo Pierre Nkuruzinza adzapikisane nawo kachitatu paudindo wa pulezidenti, mpingowu uyimitsa  thandizo lomwe unalonjeza kuti uthandiza pa chisankhocho.

Padakali pano zipani zotsutsa boma m’dzikomo zati sizidzavomereza zotsatira za chisankhocho, ngati boma la dzikolo lipitilize ndi ganizo loti chisankhochi chichitikebe pa 5 mwezi wa mawa.

Pulezidenti wa dzikolo akupitiliza kunena zoti iye ndi wokonzeka kudzapikisana nawo pa chisankhochi ngakhale kuti anthu sakugwirizana ndi ganizo lake.

Anthu oposa makumi atatu ati ndi omwe aphedwa pa ziwonetsero zokwiya ndi ganizo la mtsogoleriyo.

Malamulo a dziko la Burundi akuti samalola Pulezidenti kulamulira zaka zoposa khumi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>