Mpingo wa Katolika wati ukufunitsitsa kuti boma la Malawi liwunikenso bwino njira zomwe zidakhazikitsidwa poyendetsa ntchito zamaphunziro pofuna kuti maphunziro apite patsogolo m’dziko muno.
Mkulu woyang’anira ntchito za maphunziro ku likulu la Mpingowu kuno ku Malawi a Cleopas Mastara ndiwo anena izi potsiriza pa mkumano omwe ofesi yawo mogwirizana ndi ofesi yowona za chilungamo ndi mtendere (CCJP) inakonza ndi cholinga chofuna kumva maganizo a anthu pa momwe maphunziro akuyendera.
Msonkhanowu unachitikira mi nzinda wa Mzuzu.
“Ofesi yathu ikuyembekezeka kumva maganizo m’zigawo zonse za dziko lino ndipo zotsatira zake tikazipereka ku boma ndi cholinga chofuna kupeza njira zokonzera mavuto ena omwe akupangitsa kuti maphunziro alowe pansi”, atero a Mastara.
Pa mkumanowu panafika akuluakulu oyendetsa ntchito za maphunziro, aphunzitsi ndi ena ambiri.
Mwazina nthumwizi zadandaula kuti njira yatsopano ya kaphunzitsidwe ka ana m’sukulu za pulaimale yotchedwa PICA sikakupindulira anawo ndipo pakufunika kuti boma lisinthe njirayi.
M’mawu ake mkulu woona za maphunziro ku Mzuzu Diocese a Joseph Longwe ati masiku ano ophunzira akumaona ngati kulangidwa kwa mtundu uliwonse ndi aphunzitsi ndikumphwanya ufulu wawo.
Nthumwi zamvana kuti boma likuyenera kuti likweze malipiro a aphunzitsi ndi cholinga choti adzikhala ndi chidwi pa ntchito yawo.
Mkumano ngati umwewu ukuyembekezekanso kuchitika m’maboma a Balaka Lilongwe ndi Mulanje.