Akhristu a mpingo wakatolika m’dziko la Nigeria awalimbikitsa kuti apemphelere wa nsembe wa mpingo wakatolika amene anagwidwa ndi anthu ena osadziwika m’dzikomo pa 8 mwezi uno.
Wansembeyo yemwe akudziwika ndi dzina loti Bambo Emmanuel Aking’lbade a matumikira ku Parish ya St Benedect yomwe kupezeka m’dera la Ido-Elklt m’dzikomo.
Malingana ndi ena mwa omwe anali limodzi ndi bambowa patsikuli anthuwo anauza bambowo kuti awapatse ndalama zokwanira 20 Million Naira zomwe ndi zochuluka kwambiri .
Padakalipano ma Episkopi a mpingo wakatolika m’dzikomo alimbikitsa akhristu a mpingowu kuti apempherere bambo-wa kuti zigawenga zomwe zawagwilazo ziwatulutse, komanso kupemphelera zigawengazo kuti zitembenuke mitima ndi kuleka kuchitira anthu za upandu zosiyanasiyana.