Kapani ya candlex mdziko muno yankhazikitsa makina atsopano wopangira katundu ngati njira imodzi yofuna kuti mitengo ya katundu wawo inkhale yotsika mtengo.
Mkulu woona zopanga ndikugula katundu kukapaniyi Fredric Shangaya wati ,kampaniyi yachita izi potengera kukula kwachiwelengelo cha makasitomala womwe amagwilitsa tchito katundu wawo.
Iwo anati katundu wawo yemwe amagwilitsidwa tchito kwambiri pa ntchito yapankhomo akuyenera kuti ankhale ndi mtengo woti aliyense anthe kugula posatengera kupeza kwake.
“Ife ngati a Candlex timankhulupilira kuti popanda ma kasitomala sitingankhalepo ndiye tikamapanga zinthu kaya ndi Sopo kaya Mafuta chinachilichonse, kasitomala amakhala patsogolo”,anatero a Fredrick.
Iwo anathokoza Ambuye chifukwa cha phindu limene kapani yawo ikupeza, ananthokozanso Amalawi ndipo alonjedza kuti apitiliza kuwapatsa katundu wabwino.