Bungwe la Association of Member Episcopal Conferences in Eastern Africa (AMECEA) layamikira Pulezidenti wa dziko la Malawi Prof Peter Mutharika chifukwa chakupambana kwake pa chisankho chomwe chinachitika mwezi wa May.
Bungwe la AMECEA lomwe likuchita msonkhano wake mumzinda wa Lilongwe lanena izi kudzera kwa wapampando wake kiepiskopi Tarcisius Ziyaye omwe ndi Akiepiskopi wa Akidayosizi ya Lilongwe pa mwambo wa misa yotsekulira msonkhano wa nambala 18 wa bungweli omwe unayamba pa 16 July ndipo uzatha pa 26 July.
"Mmalo mwa bungwe la AMECEA ndi ndiyamikire Pulezidenti wathu chifukwa chopatsidwa udindo umenewu ndi a Malawi, ife a bungwe la AMECEA tikulonjeza kukupemphererani pamene mukulamulira dziko lino," anatero Ambuye Ziyaye.
Ambuye Ziyaye anathokozanso Prof Mutharika chifukwa chokhala nawo pa mwambowo zomwe anati zinasonyeza kuti a Malawi alandira bwino alendo a mmaiko osiyanasiyana omwe afika ku msonkhanowu.
Poyankhulaponso mogwirizana ndi zomwe Ambuye Ziyaye anayankhula,wapampando wa bungwe la Episcopal Conference of Malawi Ambuye Joseph Mukasa Zuza, anati mpingo onse wa katolika ku Malawi ukuyamikira Prof Mutharika chifukwa chopambana pa chisankho cha pulezidenti chomwe chinali chokhacho choyamba chapatatu.
"Mmalo mwa mpingo wa katolika ku Malawi ndikulonjeza kuti tigwira ntchito limodzi ndi boma lanu potukula dziko lino," anayankhula motero Ambuye Zuza.
M’mawu ake Pulezidenti Mutharika anathokoza mpingo wa katolika wa ku Malawi ndinso bungwe la AMECEA chifukwa chothandiza pa chitukuko cha mmaiko omwe ali pansi pa bungweli maka m’magawo a umoyo ndi maphunziro.
"Boma langa limayamikira ntchito zomwe mpingo wa katolika ukuzigwira mmaiko akumadzulo kwa Africa ndipo ndikofunika kuti tonse tizigwirira ntchito limodzi," a Mutharika anatero.
Pulezidenti Mutharika anafuniranso mafuno abwino nthumwi za ku msonkhanowo kuti ukhale wopambana.
Ena mwa akulu akulu omwe anafika pa mwambo wotsekulira msonkhanowu anali Cardinal John Cardinal Njue amdziko la Kenya, wachiwiri kwa pulezidenti a Saulos Chilima, mtsogoleri wachipani cha Malawi Congress Dr Lazarus Chakwera komanso mtsogoleri wachipani cha People's Progressive Movement Mark Katsonga Phiri.
Bungwe la AMECEA linakhazikitsidwa mchaka cha1961 ndipo mamembala ake ndi maiko a Eritrea, Ethiopia, Kenya, Malawi, South Sudan, Sudan, Tanzania, Uganda ndi Zambia.
Bungweli lmachita misonkhano yamtunduwu zaka zitatu zilizonse ndipo uwu ndi msonkhano wachitatu kuchitikira ku Malawi.