Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu Achiwembu Avulaza a Polisi Mdziko la Burundi.

$
0
0

Apolisi khumi ndi mmodzi avulazidwa mu mzinda wa Bujumbura mdziko la Burundi pachiwembu chomwe anthu ena anachita.

Anthuwo akuti anachita zachiwembu za mtunduwu mmalo osiyanasiyana ogwilira ntchito a polisi maka mmaboma momwe mwakhala mukuchitika ziwonetsero zosakodwa ndi ganizo lamtsogoleri wadzikolo Pierre Nkuruzinza ofuna kuyima kachitatu paudindo wawu pulezidenti.

Apolisi adzudzula magulu a zipani zotsutsa boma kuti ndi omwe akukolezera ziwembu mdzikolo.

Malinga ndi Mkonzi wankhani ku wailesi ya BBC mmaiko a mu Africa Mary Harper wati pali chiyembekezo chachikulu choti ziwembu zamtunduwu zitha kuchulukirachulukira pamene anthu mdzikolo akuyembekezeka kusankha aphungu akunyumba yamalamulo komanso pulezidenti pa chisankho chomwe chichitike mwezi wa mawa.

Magulu omenyelera ufulu wa anthu mdzikolo ati pakadali pano anthu pafupifupi makumi asanu ndi awiri aphedwa ndinso ena oposa zikwi dzana limodzi     athawa nyumba zawo.

Ndipo Zipani zotsutsa mdzikolo zati kulola pulezidenti Nkuruzinza kuti ayimenso paudindowu ndikulakwira malamulo kaamba koti walamulira kale materemu awiri.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>