Asisteri achipani cha daughters of wisdom lolemba anapereka zipangizo zosiyanasiyana zothandizira pachipatala chaching’ono cha Mayaka m’boma la Zomba.
Polankhula ndi Radio Maria Malawi Sister Ireen Vito omwe anaimilira nkulu wachipanichi mdzikomuno ati cholinga chawo popereka thandizolo chinali chofuna kuthandiza anthu omwe amadalira chipatalachi chomwe chimasowa zipangizo zosiyanasiyana pantchito zaumoyo.
Nkulu oyang’anira chipatalachi Sister Emma Nazombe anati mphatso zomwe analandira ndizamtengo wapatali ndipo ziwanthandidza kupereka chinthandizo choyenelera kwa anthu amene amalandira chinthandizo pa chipatalachi.
“mwachitsazo panopa talandila otokeleti,otokeleti imeneyi itinthandiza ifeyo kugwilitsa ntchito zinthu zimene zili zomphikidwa bwino moti tilewa kupeleka matenda kuchoka kwa patient(wodwala) wina kupita kwa patient wina komanso anthu wogwira ntchito mchipatala chifukwa zinthu zimenezi zitinthandiza kuti zinthu zimenezi zizinkhala zomphikidwa bwino.”
Ndipo anawonjezera ponena kuti Makina wothandizira kupuma omwe alandira athandiza kuti anthu amene akufunika mpweya adzinthandizidwa makamaka ana womwe amabadwa ndi phuma ngankhalanso azimayi womwe amabanika kochira. Katundu yemwe asisiteriwa apereka ndi wandalama zoposa 12 miliyoni kwacha.