Khonsolo ya boma la Phalombe yalonjeza kuti ipereka kuboma madandaulo aanthu am’bomalo omwe atopa ndi vuto lakusowa kwa chipatala chachikulu.
Akuluakulu akukhonsoloyi anena izi lolemba atalandira kalata yamadandaulo yomwe anthuwa anakapereka pambuyo paziwonetsero zabata zomwe anakonza mogwirizana ndi nthambi ya Chilungamo ndi Mtendere mumpingo wa Katolika mu Arkidayosizi ya Blantyre.
Ndipo Cholinga cha ziwonetserozo chinali chofuna kukumbutsa boma za mavuto a zaumoyo omwe anthu m’bomalo akukumana nawo kaamba kosowa chipatala chachikulu.
Wapampando woimilira anthu wodandaula a Kingsley Pulala anati ali ndi chinkhulupiliro chonse kuti pulezideti Muntharika anthandiza pavutoli.
“Ndili ndi chikhulupiliro kuti boma ili timanena kuti its alistening government( boma lova madandaulo) ndiye ndiri ndichinkhulupiliro kuti apapa atiyankha, nkhani yaikulu tikufuna kuti apulezideti alowelelepo chifukwa nkhani imeneyi yankhala akukambirana ku parliament (nyumba yamalamulo) kuyambira mma 2005.”Anatelo a Dandaula.
Poyankhulapo atalandira Kalatayo mmalo mwa Bwanakumbwa wa Bomali, wapampando wa zaumoyo komanso chilengedwe a Francis Nunkhazingwe anatsimikira anthuwo kuti kalatayo ayesesa kuti ikafika kwa Bwanankubwa ,ndipo kuti bwanakuyo achite chontheka kuti kalatayo ikafike kwa purezidenti.
“ine ndikuwatsimikizira abale anga wokhala kuno ku Phalombe kuti petition (kalata) imene atipasa iyenela kukafika kwa puresizidenti chifukwa ndiganizaso kuti sikoyamba kupelekedwa kwazimenezi, komabe ngati anthu okhuzidwa kuno tiwonesesa kuti a Dc (bwanakumbwa) atumize kalata imeneyi kuti ikafika kwa pulezidenti,”Anatelo a Nunkhazigwe.
Iimodzi mwa bungwe lomwe linatenga nawo ngawo padziwonetselopo linala la CCJP, ndipo kudzera mwa nkulu woona zamaphudziro komanso ulamuliro wabwino Apatrick Chiphwanya anati chinthu china chofunikira kwambiri chikupelewela mbomalo.
“Ku Phalombe kuno takhala tikupanga pulojekiti yonkhudza Demokalesi, ufulu wa anthu, ufulu wachibadwidwe, ndiye kudzera mupulojekiti imeneyi anthu akuno vuto lomwe ali nalo lachipata akhala akupempha boma, mwina mwankhala mukunva ku parliament, mma news zankhala zikulembedwa komano palibe chomwe chikuchitika ndiye anachiona kuti njira yabwino ndikuwadziwitsa aPulezideti kuti mwina alowelelepo.”a Patrick anatero.
Iwo anapitiliza ponena kuti kubwela kwawo kunali kugopelekeza.
Magulu osiyanasiyana kuphatikizapo a mipingo mabungwe omwe siaboma,mafumu ndinso anthu okhala m’bomalo ndi omwe anatenga nawo mbali padziwoneselozo.