Mtsogoleri wa dziko la Tanzania a Jakaya Kikwete ati kusankhidwa kwa Papa Fransis kuthandiza kwambiri kupititsa patsogolo chikhulupiliro pakati pa a Katolika komanso anthu onse kaamba koti moyo wa Papayu ndi okomera anthu osauka.
A Kikwete ati kusankhidwa kwa Papa Fransis kukhala mtsogoleri wa Mpingo wa katolika kuthandiza kwambiri kulimbikitsa chikondi pakati pa anthu osauka pa dziko lonse lapansi.
Chikatala chomwe boma la dzikolo latulutsa pofunira mafuno abwino papa Fransis chati kusankhidwa kwa Papayu ndi chitsimikizo choti Mpingo wa Katolika pa dziko lonse la pansi ukumukhulupilira Papa watsopanoyu kamba ka moyo wake odzichepetsa komanso kukonda anthu osauka.