Msonkhano wachiwiri wapachaka wa bungwe la maepiscope a mpingo wa katolika la Episcopal Conference of Malawi (ECM) wayamba mudzinda wa Lilongwe.
Malinga ndi chikalata chomwe bungweli latulutsa ,msokhanowu wayamba lolemba ndipo utha lachisanu.
Nthumwi ku kumsokhanowu zikukambirana nkhani yokhudza zokonzekera za chikondwerero choti Seminary ya Kachebere yakwanitsa zaka 75,malamulo owona za chipembedzo mumpingo ndiponso nkhani zokhudza msonkhano wa Sinodi.
Ma Bishopuwanso akambirana malipoti ochokera mmakomishoni, mmadipatimenti ndi mapulojekiti osiyanasiyana amu`mpingo wakatolika.