Popitiliza kusinkhasinkha nkhani zokhudza banja, mtsogoleri wampingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco wati ndi okhudzidwa ndi mavuto omwe amachitika mmaanja maka amene amaika ana pamavuto.
Iye amalankhula izi pazolankhulalankhula zomwe amakhala nazo lachitatu lilonse pabwalo la St Peters Square kulikulu la mpingowu ku Vatican.
Papa Francisco wati amadziwa kuti palibe banja limene limangoyenda popanda mavuto maka chifukwa chosiyana maganizo pakati pa makolo zomwe zimachititsa kuti asiyane ndikukafuna mayankho a mavuto awo kwina.
Iye wati vutoli likakula limaika ana pamavuto.Iye anathokoza Mulungu chifukwa cha mabanja omwe amatha kupilira pa mavuto chifukwa chokhulupilira Mulungu.