President wa Radio Maria Malawi a Nicholus Chonde wayamikira akhristu omwe akhala akuchitapo kanthu pothandiza Radio Maria Malawi m’masiku a Mariatona kuyambira pa 15 May mpaka pa 27 June 2015 yomwe imachitika ndi cholinga chofuna kupeza thandizo la ndalama zoposera 15 Million Kwacha zothandizira ntchito yomangira Transmitter m’boma la Thyolo. .
A Chonde amalankhula izi loweruka pa mwambo wotsekera International Mariatona-yu ku phiri la Michiru ku Chilomoni mu Arch diocese ya Blantyre.
Iwo ati ali ndi chikhulupiliro kuti thandizo lomwe akhristu achita lithandiza wailesiyi kukwaniritsa zolinga zake.
Polankhula wapampando wa abwenzi a Radio Maria Malawi mu Archdiocese-yi a Joseph Rappozo ati abwenzi a wailesiyi mu Archdiocese-yo apitiriza kudzipereka pothandiza wailesiyi kuti ikwaniritse zolinga zake
M’mawu ake mkulu woona ntchito za ma pologalamu ku wailesiyi Bambo Joseph Kimu alimbikitsa abwenzi a wailesiyi mdziko muno kuti azionetsanso chidwi potenga nawo mbali yokonza komanso kuwulutsa ma pologalamu osiyanasiyana pogwiritsa ntchito luso ndi mphatso zomwe ali nazo.