Malipoti ochokera mdziko la Tunisia ati munthu yemwe wapha anthu 38 pa malo ena okopera alendo lachisanu lapitali mdzikolo anathandizidwa ndi anthu ena omwe sakudziwika kuti achite chiwembucho.
Malipoti ati anthu makumi atatu mwa anthu omwe adafa pa chiwembucho ndi mzika za mdziko la Britain.
Padakali pano dziko la Britain latumiza apolisi oposa khumi ndi asanu mdziko la Tunisia kuti akathandizire pa ntchito za chitetezo pomwenso dzikolo likuwunika momwe chiwembucho chidachitikira.
Dziko la Tunisia lalengeza kuti litseka mizikiti pafupifupi makumi asanu ndi atatu 80 yomwe likuyiganizira kuti anthu omwe amapemphera mmizikitiyo amalimbikitsa mchitidwe wa ziwawa mdzikolo.
Zigawenga za Islamic State IS zalengeza kuti izo ndi zomwe zachita chiwembucho.