Ntchito yoponya voti pa chisankho cha aphungu ndi makhansala mdziko la Burundi siyidayambe bwino, anthu omwe sakudziwika ataponya mabomba mmalo oponyera voti mumzinda wa Bujumbura ndinso mmadera ena mdzikolo.
Izi zikuchitika pamene anthu akupitiriza kuchita ziwonetsero pokwiya ndi ganizo la mtsogoleri wa dzikolo Pierre Nkurunzinza lofuna kuyima kachitatu paudindo wa pulezidenti pachisankho chomwe chichitike mdzikolo pa 15 mwezi wa mawa.
Zipani zotsutsa komanso mabungwe omwe siaboma akana kutenga nawo mbali pachisankhochi, boma litalephera kumvera malangizo a mabungwe osiyanasiyana omwe amapempha kuti chisankhochi chiyambe chayimitsidwa pofuna kukonza mavuto omwe anthu mdzikolo akudandaula.