Maepiskopi a mpingo wa katolika mdziko la United States ati akuyembekezera kuti ulendo wa Papa Francisco mdzikolo womwe uchitike mmwezi wa September udzakhala wopindula.
Malipoti a Catholic News Agency ati pa ulendo wa masiku asanu ndi anayiwa pambuyo poyendera dziko la Cuba komwe akakumane ndi atsogoleri a zipani zosiyanasiyana, Papa Francisco adzakayenderanso madera ena atatu mdziko la United States.
Maepiskopi am’maderawa atamva izi anali okondwa kaamba koti anachiwona chinthu cha mtengo wapatali kuyenderedwa ndi mtsogoleriyu.
Papa Fransisco akatsirizira ulendo wakewu pokumana ndi President wa dzikolo Barrack Obama.