Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco lachiwiri anakachezera mtsogoleri wakale wa mpingowu wopuma Papa Benedicto wa XVI yemwe wapita ku nyumba ya Papa ku dera la Castel Gandolfo mdziko lomwelo la Italy.
Malipoti a wailesi ya Vatican ati Papa Francisco amakafunira mafuno abwino Papa Benedicto pa ulendowo womwe akuyembekezeka kukakhalako sabata ziwiri.
Mtsogoleriyo anachita kupempha Papa wopumayo kuti mwezi wa July akacheze ku nyumbayo kamba koti yakhala nthawi yayitali osagwira ntchito ndipo Papa wopumayu anavomera.