Asilikali a kummwera kwa dziko la Sudan awotcha asungwana pafupifupi 170 kamba ka nkhondo ya pa chiweniweni yomwe ikuchitika mdzikolo.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC asungwanawa atagwidwa ndi asilikaliwa ena mwa iwo anagwiliridwa ndipo pa mapeto ake anawaotcha.
Boma la dzikolo lati silikugwilizana ndi lipoti lomwe bungwe la United Nations latulutsa lokhudza nkhaniyi ndipo ilo lati lifufuza gwero la mchitidwewu.
Nkhondo ya pachiweniweni yomwe yakhala ikuchitika mdzikolo inayamba mu chaka cha 2013 pulezidenti wa dzikolo Salva Kiir atachotsa wachiwiri wake Riek Marshal kaamba kotsogolera gulu lofuna kuwukira pulezidentiyo.