Makampani opanga zakumwa a Carsberg Malawi komanso Southern Bottlers apereka katundu osiyanasiyana othandizira pachipatala chachikulu cha Zomba.
Popereka katunduyu mneneri wa kampani ya Southern Bottlers Mayi Towera Munthali ati kampani yawo yapereka thandizoli powona mavuto omwe chipatalachi chikukumana nawo pantchito yake yothandiza anthu.
Mayi Munthali ati malinga ndi kafukufuku wawo anapeza kuti ntchito zina pa chipatalacho sizikuyenda bwino kamba kakuchepa kwa zipangizo.
Polankhulapo mkulu wa chipatalacho Dr Mathias Joshua ati katunduyu wabwera pa nthawi yake kamba koti chipatalachi chikukumana ndi mavuto ambiri monga kusowa kwa mankhwala komanso zipangizo zoyezera matenda osiyanasiyana.
Katundu yemwe waperekedwa pa chipatalachi ndi wokwana 77 miliyoni kwacha ndipo ma kampaniwa akugwira ntchitoyi mothandizidwa ndi mabungwe a City Hope International komanso Medi Care a mdziko la Amerika mu zipatala za mdziko muno za Ekwendeni m’boma la Mzimba, Queen Elizabeth mu mzinda wa Blantyre komanso Zomba Central.