Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

A VUWA KAUNDA AMANGIDWASO POMWE AMAFUNA KUPITA KU ULAYA

$
0
0

 M'modzi wa akuluakulu a chipani cha Democratic Progressive DPP a Symon Vuwa Kaunda omwe anatulutsidwa pa belo sabata yangothayi awamanganso pa 17 March 2013 pomwe amafuna kukwera ndege kupita ku Ulaya.

A Kaunda ndi anthu ena akuwazenga milandu yosiyanasiyana kuphatikizapo yofuna kulanda boma potsatira imfa ya pulezidenti wa kale wa dziko lino malemu Bingu wa Mutharika chaka chathachi.

 Mneneli wa apolisi m'dziko muno a Rhoda Manjolo atsimikiza za nkhaniyi.

 "Apolisi amanga a Kaunda pa bwalo la ndege la Kamuzu International pomwe amafuna adzikwera ndege kupita ku Brussels m'dziko la Belgium kukachita nawo msonkhano wa aphungu a kunyumba ya malamulo chonsecho milandu yawo ikupitilira",atero a  Manjolo.

 Oweruza milandu kubwalo lalikulu la High Court A Ivy Kamanga akuti anapereka chilolezo kuti a Kaunda akhoza kupita ku Belgium koma iwo sanauze apolisi ndipo awamanga.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>