Unduna wa za umoyo wati anthu 5 miliyoni ndi omwe anadwala matenda a malungo chaka chatha ndipo mwa anthuwa 5 Sauzande 5 handirede adamwalira ndi matendawa ngakhale kuti matendawa ndi opeweka komanso ochizika m'dziko muno.
Mlembi wamkulu mu undunawu Dr.Charles Mwansambo ndi omwe anena izi pamwambo okhazikitsa kafufukufu wa chaka cha 2012 owona za matendawa omwe umachitikira mu nzinda wa Lilongwe.
Dr Mwansambo ati zotsatira za kafukufukuyo zithandiza kupereka chithunzithunzi cha momwe ntchito yolimbana ndi matendawa ikuyendera komanso kuwona zomwe zakwanilitsidwa pa nkhani yolimbana ndi matenda a malungo m'dziko muno.
Undunawu watinso ndi okondwa ndikutsika kwa chiwerengero cha ana osaposera zaka zisanu omwe anagwidwa ndi matendawa.
“Tili okondwa kuti chiwerengero cha ana omwe anagwidwa ndi matendawa chatsika kuchoka pa 43 kufika pa 28 pa zana lililonse”, atero Dr Mwansambo.
Undunawu wapemphanso magulu onse omwe amathandiza boma pantchito ya za umoyo kuti aganizirenso zodzipereka kwatunthu pantchito yolimbana ndi matendawa.